Yamikani Samuel wati tsopano watulutsa kanema wanyimbo yake ya Kuyenda ndi Yesu

By Chisomo Phiri

Yamikani Samuel yemwe ndi oyimba wa chamba cha nyimbo za uzimu mdziko muno wati tsopano watulutsa kanema wanyimbo yake ya uzimu yatsopano yotchedwa ‘Kuyenda ndi Yesu’ yomwe anayiyimba ndi mzake wina otchedwa MacMillan Demataya.

Malinga ndi Samuel,uthenga waukulu omwe uli mnyimbo yatsopanoyi ndiwokumbutsa anthu kuti kuyenda ndi yesu ndikwabwino chifukwa cha zimene amatichitila.

Yamikani Samuel



Oyimbayu yemwe panopa akukhala mdziko la South Africa anati chomwe chinamupangitsa kulemba nyimboyi ndichakuti iye Mulungu anamupambanitsa muzinthu zowopsa zosasimbika ndipo kuti anawona ukulu wa Mulungu pamoyo wake.

Iye anati kanema wanyimboyi anajambula yekha.

“Kwa amene akufuna kumvera nyimbo yanga yatsopayi atha kuyipeza pa YouTube komanso pa webusaiti wa  Golden City Tower,” anatero Samuel.

Iye analonjeza omwe amakonda kumvera ndi kuonera nyimbo zake kuti  ayembekezele nyimbo zambiri kutsogoloku.

Samuel anapempha okonda nyimbo zakewa kuti asasiye kutelo poti izi zimamupatsa chilimbikitso.