A DPP akufuna kubweletsa chisokonezo poyika m’bale wathu Saulos Chilima- Zatero Mbadwa Zokhudzidwa

By Joseph Banda

Gulu lina lomwe likuzitchula kuti ‘Mbadwa Zokhudzidwa’ lati chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) chamema achinyamata ena omwe chikufuna kuti akayambitse chisokonezo mawa lino pa mwambo oyika m’manda thupi la yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko Dr. Saulos Chilima kumudzi kwawo ku Ntcheu.

Kudzera mchikalata chomwe ife taona, gululi lati lili ndi umboni onse pa izi.

“Ife monga Mbadwa Zokhudzidwa, tikufuna kuima pamodzi ndi mtundu onse wa Malawi pamodzi ndi Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera polira abale ndi alongo Including the Vice President Rt. Honourable Dr Saulos Klaus Chilima, amene ataya miyoyo yawo pangozi ija ya ndenge imene idachitika pa 10 June 2025 Ku Chikangawa.

Mbadwa zokhudzidwa



“Ife Mbadwa Zokhudzidwa tapezapo zinthu zingapo zimene ngati sitingalankhulepo ndiye kuti sitichita bwino pofuna kulemekeza moyo ndi Khalidwe la Dr. Saulos Klaus Chilima zomwe adaonesa pokhala dziko lapansi lino.

“Ndizomvetsa chisoni komanso zochititsa manyazi kuti pali anthu ena andale, maka maka a DPP omwe akufuna kutchukilapo pa maliro a Saulos Chilima. Tilinawo umboni okwanila ndipo tikudziwa anthu onse a DPP omwe akupereka ndalama kwa anyamata kuti akanyazitse President Chakwera ku maliro a Chilima ku Nsipe mawa.

“Tawawona akujijilika ku siwa kufuna kukhala ngati kuti amamukonda Saulos pomwe ndiwomwewa amamunyoza, kumunyazitsa, kumutukwana Saulos.

“Pano watisiya, akufuna akhale angelo.
Ife ngati Mbadwa Zokhudzidwa tapeza kuti azipani zotsutsa afuna kuti apangirepo ndale zawo pa Maliro amene agwera dziko lino,” latero gululi mchikalata chake.

Gululi lati laonapo ma audio clip akutuluka kuchokera kwa a  Ntanyiwa a Limpopo FM omwe amakhalira ku dziko la South Africa namakamba nkhani zamabodza ndikufuna kuononga mbiri ya anthu ena kuphatikizapo mtsogoleri wadziko lino motumidwa ndi a zipani zotsutsa amene amakatengako ndalama kudzera kwa munthu wina amene amakhala ku South Africa koma adali mugawo limodzi la chitetezo Cha Mtsogoleri wakale  wadziko lino  Prof Arthur Peter Mutharika.

“Iyeyo amalumikiza ma wire pakati pa anthu aku DPP ndi Limpopo FM.
Anthuwa akungofuna kudzetsa mkwiyo kwa mzika za Malawi ponena zinthu za mkutu. Mbadwa Zokhudzidwa zapeza kuti a zipani zotsutsa ndiwo akhala akukolezera kuti a Chipani Cha UTM azipanga zithu mokwiya poperekera zida kuti anthu adziyimba nyimbo zonyoza a Chakwera zomwe sizingakondwereste mzimu wa Dr. Chilima.

“Dr. Chilima adali mkatolika weni weni osachita nawo mapokoso opanda mzeru.

“Mbadwa Zokhudzidwa zapeza kuti a zipani zotsutsa apeza njira yofuna kutchukirapo muzipani zawo pofuna kubweresa mabodza ochuluka kuti anthu adane ndi a Chakwera.

“Tamva kuti akufuna kuti a Peter Mutharika akapita ku maliro asakagwirane chanza ndi aliyense kapena kumwa madzi amene akapatsidwe ati angakawaphe. Za ziii zeni zeni. Mutharika amapita ku maliro?

“Tikudziwa kuti zonsenzi mkufuna kupeza zifukwa zoti asakapezeke ku Maliro a Dr. Chilima. Koma a Malawi akudziwa kale kuti inu simupita ku Maliro,” chaonjezera chotele chikalatachi.

Ndipo chapitiliza kunena kuti :”Imfa ya Dr.Justin Malewezi amene adakhalapo Vice President wa dziko lino la Malawi mu utsogoleri wa Dr. Bakili Muluzi APM adabwera?

“Maliro a mayi Annie Muluzi Mayi awo a Dr. Atupele Muluzi, amene adali running mate wanu mu 2019, mudabwera?

“Maliro Vice President wanu Dr. Goodal Gondwe, mudakakamizidwa tsiku lomaliza pomwenso mudakafika mochedwa osawona nkhope.

“Maliro senior chiefs mdziko muno including a Chimaliro aku Thyolo kumene amacholera APM, mudapita?  Mdziko muno mudachitika maliro a senior Chief Kapoloma amene adali related to former President wa dziko lino Dr Bakili Muluzi ku Liwonde koma a Peter Mutharika okhalira ku Mangochi sadapezeke so.

“Chimene chikhale chachilendo ndi chiti kuti APM akalephere kupita ku maliro a Dr Klaus Chilima

“Dr Saulos Klaus Chilima sadali munthu amene amachitidwa provoke so easily and react to carelessly.

“Mulemekezeni. Wakhala moyo wa chete kuchokera pamene Chipani Cha DPP chidakhala chikumuchita provoke. Mwachitsanzo adayankhapo munthawi Ina pamene a DPP adamuyamba ndikunena kuti iye ngosayamika.
Adayankha nanena kuti musati ndine osayamika chifukwa sindikuyenera kukhala ineyo okuyamikani chifukwa ndidakupezani ku opposition ndikukulowetsani m’boma, so mukuyenera kundiyamika ndi Inuyo.

“A DPP adamuchita provoke namanena kuti adamutenga akugulitsa yabooka ndipo amutsuka tsuka. A DPP adatenga mzimayi amene adachita video clip nkuwuza anthu kuti Dr. Saulos Klaus Chilima sadali wa ku Ntcheu koma ku Mozambique.

“Ndipo a DPP adamutchula kuti Iye ndi Zeze not Saulos Klaus Chilima.
Wakoma lero Saulos mumamunyoza uja? Chonde a Malawi a mzanga maka uko ku Ntcheu a Ngoni, tisalore kuti anthu a DPP atigwiritse ntchito yosokoneza maliro a Dr. Chilima.

“Mulemekezeni m’bale wanu kuti mzimu wake uwuse mu mtendere.”