Wolemba Linda Kwanjana
Dr Zikhale Ng’oma yemwe ndi nduna yowona nkhani za chitetezo chamdziko a lero inakayendera Ndende ya Maula mumzinda wa Lilongwe.
Mukulankhula kwawo, ndunayi inapempha akaidi okhala mndende imeneyi kuti alembetse mwaunyinji kuti azathe kuvota pa chisankho chomwe chikubwera chaka chamawa.
Azikhale anatsimikizira akaidi onse pamalowa kuti boma likupanga chilichonse chotheka kuti chiwerengero cha akaidi chomwe ndi chokwera kwambiri , chitsike.
Ndunayi inapereka ndalama zokwana K5Million komanso sopo okwana ndalama zokwana K2Million.
Mukulankhula kwawo mukulu wandende mdziko muno a Masauko Wiscot adathokoza ndunayi kamba ka thandizo lomwe laperekedwa pamalopo.
A Wiscot adati, ndalama yomwe alandira ithandiza kugula zakudya pandende imeneyi.