Wolemba Mtolankhani Wathu
Mamembala a chipani cha Malawi Congress (MCP) m’busa Mwai Kamuyambeni komanso a Samson Nthenga atsutsa malipoti oti alowa chipani cha UTM.
Izi zikutsatira chithunzi chomwe awiriwa anajambulitsa ndi mtsogoleri wachipani cha UTM, a Dalitso Kabambe kunyumba kwao Lachiwiri sabata ino.
Awiriwa avomera kuti anajambulitsa chithunzicho pomwe anawaitana monga munthu ndi mzache poti anayamba kucheza kalekale.
Iwo ati anali odabwa kuti pomalizira kwakucheza kwao a Kabambe anawapempha kuti agwire nao ntchito ndipo m’busa Kamuyambeni ndi a Nthenga ati anangoti awayankhabe.
Titawafunsa ati mauwa anali kukana ndithu kulowa chipani cha UTM ndipo iwo ali pambuyo pachipani cha MCP.
A Kamuyambeni ati iwo adzaimira ngati phungu wa MCP dera lina m’boma la Ntcheu.
O