Tuesday, January 7, 2025
No menu items!
spot_img
HomeOpinions and AnalysisUlendo wa Pulezidenti Chakwera mdziko la UAE wabala zipatso

Ulendo wa Pulezidenti Chakwera mdziko la UAE wabala zipatso

Wolemba: Kondanani Chilimunthaka

Ulendo omwe Mtsogoleri wa dziko lino, *Dr. Lazarus Chakwera* anali nawo masabata angapo apitawa mu mzinda wa Abu Dhabi, mdziko la United Arab Emirates (UAE) wayamba kale kubala zipatso zokoma kwa a Malawi, ngakhale kuti chiyembekezo chinali choti zipatso zake ziyamba kuoneka mumwezi wa Febuluwale chaka chino cha 2025.

Malinga ndi chikalata chomwe unduna owona za mphamvu ya magetsi ndi mafuta watulutsa, ndipo chasayinidwa ndi nduna mu undunawu, a Ibrahim Matola  lachisanu pa 3 Januwale, 2025, boma la Malawi lapeza mafuta okwana matani 40,000, omwe ndi pafupifupi malitala 51.5 miliyoni a Dizilo komanso Petulo kuchokera mdziko la UAE.

Matola
President Chakwera Ku UAE



A Matola ati, iyi ndi ndondomeko yapadera pofuna kuonjezera pa mulingo omwe akubweretsa mabungwe ovomerezeka a NOCMA, PIL, komanso magulu ena omwe amatenga mafuta kunja kubweretsa mdziko muno, omwe pakatipa akumana ndi zobetchera zambiri pa ntchito yawo.

“Potsatira kulengezedwa kwa kusintha kwa ndondomeko pa kayitanitsidwe ka mafuta kuchokera kunja, yomwe adalengeza Mtsogoleri wa dziko lino, a Dr. Lazarus McCarthy Chakwera, boma la Malawi kudzera munduna owona za mphamvu ya magetsi ndi mafuta, komanso bungwe losankhika la NOCMA, tapeza mafuta okwana matani zikwi makumi anayi (40,000 metric tons), omwe ndi pafupifupi malita 51.5 miliyoni a Dizilo komanso Petulo, kuchokera ku Abu Dhabi, mdziko la United Arab Emirates” yatero mbali ina ya chikalata chomwe a Matola asayina.

Chikalatachi chati mafutawa agulidwa pansi pa mgwirizano wa maboma a maiko a Kenya ndi Malawi pogwiritsa ntchito mgwirizano omwe ulipo kale pakati pa boma a Kenya ndi Abu Dhabi, pa nthawi yomwe dziko la Malawi lili kalikiliki kuyika njira ndi ndondomeko zokhazikitsira ubale onga omwewu ndi maiko achiluya.

Chikalatachi chitsimikiziranso a Malawi kuti mafutawa afika kale pa doko la Tanga mdziko la Tanzania, ndipo kuti ayamba kufika mdziko muno lachinayi pa 9 Januwale, 2025.

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments