A Chakwera anenetsa kuti dziko lino likufunika nyumba zabwino zopirila ku ngozi zogwa mwadzidzidzi

By Linda Kwanjana

Mtsogoleli wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera watsindika kufunika kwa-kuti m’zika za dziko lino zizimanga nyumba zomwe ndizolimba komanso  zopirila ku ngozi zogwa mwadzidzidzi

Mtsogoleli-yu anati boma lake layika chidwi pa ntchito-yi pomwe ndondomeko yomanga nyumba yayambika kale pansi pa ndondomeko yotchedwa “Project 250”.

Chakwera wayakhula izi ku Lilongwe pomwe amakhazikitsa ntchito za ndondomeko-yi pomwe boma kudzela mu ma kampani m’dziko muno komanso akunja  likuyembekezeka kumanga nyumba zokwana 250,000.

President Chakwera

“Vuto la nyumba ndiralikulu m’dziko muno, ndipo ndikufuna kuthokoza azitsogoleri anzanga akale a dziko lino Dr. Joyce Banda komanso Dr. Bakili Muluzi kaamba ka ndondomeko yomangiranso nyumba anthu omwe anankhudzidwa ndi namondwe freddy, boma lino likufunitsitsa aliyense akhale ndi nyumba zabwino,” Chakwera anatelo.

Anafotokozanso kunena kuti mu ndondomeko-yi nyumba 10, 000 zoyambilila zikuyembekezeka kumangidwa ndipo kuti mwa nyumba-zi 1,000 ntchito yake inafika kale kumapeto.

Nyumba za mu ndondomeko-yi ndikuphatikizapo zomwe asilikali komanso a polisi adamangilidwa.