By Staff Reporter
Hon Zikhale Ng’oma akupitiliza ntchito yomemeza anthu kuti akalembetse mwaunyinji mu kaundula wa voti pomwe lero ali Ku Usiska Ku Nkhata-bay North Constituency.
Pa ulendowu,a Zikhale akuyenda limodzi ndi shadow MP wa Nkhata-bay Central a Ralph Mhone Komaso a Shadow MP a Nkhata-bay North Constituency a Mganda Chiume.
A Zikhale omweso ndi nduna ya chitetezo cha m’dziko,ati akuchita izi pofuna kulimbikitsa anthu kuti alembetse mwa unyinji ndikuti azavotere Dr Lazarus McCarthy Chakwera pa chisankho cha mu 2025.

Iwo ati ndikhumbo lawo kuti chipani cha Malawi Congress ( MCP) chizapeze aphungu ochuluka kuchoka m’boma la Nkhata-bay.
Lero a Zikhale akuyembekezeka kufika m’madera a Bula, Kaulasisi, Chigwere,Chipunga ndipo akachititsa msokhano waukulu pa Chikwina trading centre.
Lachisanu, ndunayi inayendera anthu aku Bwerero,Lisale, Kachenga Mlombwa ndi Chilambwe.