A Zikhale afunila zabwino Nduna Yatsopano Vitumbiko Mumba

Wolemba: Mtolankhani Wathu


Nduna yazachitetezo cha mdziko lino Dr. Ken Zikhale Reeves Ng’oma ayamikira a Vitumbiko Mumba posankhidwa kukhala nduna ya za ntchito.

A Ng’oma ati kusankhidwa kwa a Mumba ndi chitsimikizo chakuti mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus McCarthy Chakwera amalemekeza maganizo a Amalawi omwe kwa nthawi yaitali akhala akufunitsitsa kuti nzeru za a Mumba zipezeke pa mndandanda wa nduna zaboma.



“Ndikuuzeni chilungamo chakuti sindidadabwe kuti bwana (Mtsogoleri Dr. Lazarus McCarthy Chakwera) asankha a Vitumbiko Mumba kukhala nduna ya za ntchito. Vitu ndi wachichepere koma ndi mtondo pa ntchito. Wangoyenera monga katswiri. Ndikuwafunira zabwino zonse a Vitumbiko Mumba. Mulungu awatsogolere,” atero a Ng’oma.

A Mumba alumbilitsidwa paudindowu ndi President Chakwera pamwambo omwe unachitikila Ku Mzuzu