Wednesday, April 2, 2025
No menu items!
spot_img
HomeNewsChakwera adzudzula dzipani  dzotsutsa kamba kofalitsa nkhani za bodza

Chakwera adzudzula dzipani  dzotsutsa kamba kofalitsa nkhani za bodza

By Linda Kwanjana

Mtsogoleli wa dziko lino a Lazarus Chakwera adzudzula dzipani dzotsutsa boma kaamba kofalitsa nkhani zabodza pa nkhani ya kakweledwe ka katundu dziko muno.

Poyakhula ku nyumba ya malamulo a Chakwera ati pali a ndale ena kumbali yotsutsa omwe akumakolezela nkhani ya kukwela kwa katundu dziko muno pouza anthu ochita malonda kuti achite izi pongofuna kupeza mphindu pa ndale.

President Chakwera



“Akuchita kulenga khani ya kukwela kwa mitengo ya katundu kwa anthu ogulitsa zithu zosiyanasiyana m’dziko muno pongofuna kuipitsa boma langa. Koma boma langa litengapo gawo pofuna kuthana ndi onse ochita izi,” a Chakwera anatelo.

A Chakwera anati ali pa ntchito yokonzanso dziko lino ndipo sangalole kuti asokonezedwe ndi kagulu ka anthu kochepa kofuna zawo zokha kuti ziyende posayang’anila chuma ndi umoyo wa aMalawi.

Ndipo a Chakwera anapitiliza kunena kuti ngati mbali imodzi yofuna kukonzanso zithu pa khani ya mitengo ya katundu m’dziko muno, asakha a Vitumbiko Mumba kukhala nduna ya tsopano ya zamalonda ndi ma fakitale kufuna kuteteza malonda omwe aMalawi amachita tsiku ndi tsiku.

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments