Chakwera akhazikitsa ntchito yogula zipangizo zotsika mtengo

Olemba : Alfred Chauwa

Mtsogoleli wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera lero wakhazikitsa ntchito yogula zipangizo zotsika mtengo za ulimi ya chaka chino (2024/ 2025) ku Zalewa m’boma la Neno ndi mawu a chilimbikitso kwa alimi ponena kuti boma lakwanitsa kupeza feteleza okwanira anthu oposa 1 million amene ali ndi kuthekera.

Mululankhula kwawo a Chakwera ati akhazikitsa ndondomeko ya chaka chino kuti alimi apeze feteleza otsika mtengo pofuna kuti alimi omwe ali ndi kuthekera kolima chakudya athe kutelo ndithu.

Chakwera

A Chakwera ati pa zitukuko zonse zimene boma lawo likuchita anthu asanamizike kuti Chakwera sanawachitile kanthu.

“Zoti m’dziko muno muli njala palibe amene sakudziwa. Kulikonse komwe ndikumapita ndikumakumana ndi aMalawi omwe dandaulo lawo lalikulu ndi njala,” A Chakwera anatelo.

A Chakwera anapitilizanso kunena kuti alimi ndi anthu ena onse akudziwa kuti m’dziko muno muli njala imene yadza kaamba ka kusitha kwa nyengo kotelo kuti anthu omwe akuyakhula kuti Chakwera ndi yemwe wabweletsa njala mdziko muno amenewo sadziwa ulimi koma ndi anthu omwe chakudya amangochionela mmbale.

“Mlimi simungamuuze zochitika mmunda mwake chifukwa amaziona yekha. Mlimi tikamupatsa feteleza ndi zipangizo motchipa amadziwa kuti amene tamuthandiza kupeza chakudya ndi ife,” A Chakwera anaonjezela.

Mtsogoleli-yu watinso waika padela ndondomeko yakuti anthu ena omwe sangathe kupindula ndi ndondomeko anthe kupindula magawo ena popeza sikoyenela kuti madela omwe kumavuta madzi kapena kuli dothi losakhala bwino adzipindula nawo.