Olemba: Mtolankhani wathu
Mtsogoleli wa dziko lino Lazarus Chakwera wapeleka uthenga wake opepesa pa za imfa ya yemwe anali katswili pa nkhani ya zolembalemba m’dziko muno a Willie Zingani.
Mu uthenga wawo a Chakwera ndi mayi wa dziko lino Madame Monica Chakwera ati iwo ndi okhudzika ndi imfa ya a Willie Zingani.

“Kudzipeleka kwawo pa nkhani ya luso la malembedwe ndi kufalitsa nkhani dziko muno kwasiya chizindikilo chachikulu m’dziko muno. Tikulila nawo popeza tataya muthu odzipeleka, ndipo zichitochito zawo zipitilize kulimbikitsa ena,” a Chakwera atelo mu uthenga-wu.
Mtsogoleli-yu ndi mayi wa dziko lino-yu ati uthenga wa chipepeso upite kwa abale ofeledwa ndi anzawo a Willie Zingani.