Sunday, January 26, 2025
No menu items!
spot_img
HomeNationalChakwera apeza ndalama zomangira likulu la ntchito za mabwalo

Chakwera apeza ndalama zomangira likulu la ntchito za mabwalo

Wolemba: Linda Kwanjana

Boma la Malawi ndi boma la China lachiwili pa 4 September, 2024 lasaina mgwirizano wa ndalama pafupifupi MK50 billion zomwe zithandizile pa ntchito yomanga likulu la ntchito za mabwalo m’dziko muno.

Nduna ya zachuma a Simplex Chithyola Banda ndi omwe asaina ngwilizanowu m’malo mwa boma la Malawi ndipo a Chithyola ati izi zili ngati mphatso yapadela yomwe boma la China lapeleka kwa anthu a dziko la Malawi.

Ndunayi inaonjezeranso kuti thandizoli lithandiza kuonjezera kudzukanso kwa dziko la Malawi.

Nduna ya zachuma Simplex Chithyola Ku China



Poyakhula atasaina ngwilizanowu a Chithyola anati mtsogoleli wa dziko la China a Xi JinPing anauza mtsogoleli wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera za thandizoli pa mkumano omwe anali nawo lachiwili m’mawa.

“Ndili okondwa kusaina ngwilizanowu m’malo mwa a Malawi, zomwe zithandizile kuti a mabwalo anthu adzitha kugwila ntchito m’malo abwino kuphatikizapo malo oweluzila milandu zomwe ndi khani yabwino.

“Udindo okuti ntchito yomanga malowa omwe adzakhale ku Lilongwe pafupi ndi nyumba ya malamulo tsopano ili m’manja mwa unduna wanga kuonetsetsa kuti anthu onse okhudzidwa afikilidwa ndikuti zonse zapelekedwa kuti ntchitoyi iyambe pompano,” Chithyola anatelo.

A Chithyola Banda anati kupatula kuti ntchitoyi isitha maonekedwe a m’zinda wa Lilongwe ilinso ndikuthekela kokweza kapezedwe ka chuma dziko lino pomwe a Malawi ambili alembedwe ntchito komanso kupatsidwa mwayi opelekela zofunikila pa ntchitoyi.

Chithyola anatinso kudzipeleka kwa dziko la China pa ntchitoyi kukubwela kaamba ka utsogoleli wa maso mphenya omwe tsogoleli wa dziko lino alinawo ofuna kumanga ma ubale abwino ndi maiko ena.

Posaina mgwilizanowu m’maloĝ mwa dziko la China a Long Zhou yemwe ndi kazembe wa dziko la China kuno ku Malawi, wati aonetsetsa kuti ndondomeko yonse yayenda mwadongosolo lake ndikuti ubale wa maiko awiliwa ukukulilakulilabe.

Kusaina ngwilizanowu kunachitika pomwe dziko la China likuchititsa m’sonkhano otchedwa Forum on China-Africa Cooperation (FOCAC) wa chaka chino komwe mtsogoleli wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera akutenga nawo mbali.

M’sonkhanowu mwa zina ukufuna kuumbanso ma ubale omwe dziko la China ndi maiko a ku Africa ali ku khani ya zamalonda, za mphamvu za magetsi komanso malonda ndi za ulimi mwa zina pofuna kukweza masophenya a 2063 omwe maiko a mu Africa alinawo.

Mkumano ngati uwu unakhazikitsidwa m’chaka cha 2000 pofuna kulimbikitsa maubale a dziko la China ndi maiko a mu Africa ndipo umachitika pakatha dzaka zisanu ndi chimodzi.

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments