By Linda Kwanjana
Mtsogoleri wadziko lino lero pa 9 September, 2024, anali ku chigwa cha Shire komwe anakagwira ntchito zingapo.
Mwazina a Chakwera anakayendera ulimi wa ziweto omwe banja lina lotchedwa Issa likupanga mboma la Chikwawa uku ndi kwa mfumu yaikulu Ngabu
Atamaliza ulendo oyendera ulimi wa ziweto umenewu a Chakwera anapitanso m’mudzi mwa Nguluwe mfumu yaikulu Mbenje ku Nsanje komwe mwazina anakayatsa magetsi aja amatchedwa kuti Malawi Rural Electrification Programme (MAREP) ya gawo 9.
Ali kumeneko mfumu yaikulu Chimombo anayamikira Chakwera kamba koyambitsa ntchito ya MAREP yomwe anati ilumikiza manyumba okwana 300.
Mfumu Chimombo mukuyankhula kwawo anati kwacha kudela kwa Mfumu yaikulu Mbenje chifukwa choti kwawala
Mtsogoleri ameneyu adakachezanso ndi aphunzitsi onse amboma la Nsanje ndi Chikwawa maka aja amati ma headteachers pa Ngabu Secondary ndi cholinga choti amve mavuto omwe iwo akupeza.
Atachoka pamenepo a Chakwera anakacheza ndi onse ochita malonda a m’boma la Nsanje ndi Chikwawa ndipo uwu ndi umene udali mkumano wawo omaliza.
Koma ali mnjira kuchokera kwa Mbenje a Chakwera anaima pa Solijeni pomwe anayankhula ku chinamtindi cha wanthu.
Mukuyankhula kwawo a chakwera omwe adalinso ndi Mai Wafuko, a Monica Chakwera adalamula ADMARC kuti ibwere ku chigwa cha Shire kuti idzatsekule misika ndi cholinga choti a Malawi okhala mdelari asafe ndi njala.