By Linda Kwanjana
Mtsogoleli wa dziko lino Lazarus Chakwera ali mu m’zinda wa Beijing ku China pomwe akuyembekezeka kukhala nawo pa m’sonkhano wa maiko pafupifupi 53 a mu Africa pomwe akhale akukambilana momwe angapititsile patsogolo ntchito za malonda, kulimbikitsa ubale, komanso chitetezo pakati pa dziko la China ndi maiko a mu Africa.
Pamene m’sonkhano-wu wayandikila, dziko la China latsimikizila kukonzeka kwake kufuna kuonetsetsa kuti ma ubale a dzikoli ndi maiko a mu Africa ndiokhazikika pofuna kufikila kukonza tsogolo lowala.
Mwa zina dziko la China likufuna kupeleka uthenga ku dziko lapansi pa kukonzeka kwawo pofuna kungwila ntchito limodzi kukonzanso kayendetsedwe ka zithu m’maikowa.
Poyakhula pa m’sonkhano wa olemba khani, wachiwili kwa nduna yoona ma ubale a dziko la China ndi maiko ena a Chen Xiaodong wati kudzela m’maubale maiko atha kuthana ndi mavuto omwe alipo m’maikowa ndikuonetsetsa kuti chitukuko chikufikila aliyense.
Dzikoli likufuna kukhazikitsa kumvetsetsa kwa maubale pakati pa maikowa.
Pa mkumano-wu otenga mbali akhale akukambilana khani zokhudzana ndi za chuma, kukhazikika pa chitukuko komanso za malonda pakati pa maiko a mu Africa ndi dziko la China.
Mkumano-wu unakhazikitsidwa m’chaka cha 2000 ngati mbali imodzi yolumikiza dziko la China ndi maiko 53 a mu Africa ndipo mkumano-wu ndi wachi nambala 8 kutsatila mkumano wa posachedwapa omwe unachitikila m’dziko la Senegal mu 2021.