Chakwera wakonzeka kulamulanso mpaka 2030

Wolemba: Linda Kwanjana

Mtsogoleli wa dziko lino  Dr Lazarus Chakwera wati pamene a Malawi ambili akhala akuona zitukuko zomwe iye akupanga kuphatikizapo kubwezeretsanso ntchito za njanji zomwe zinafa zaka 20 zapitazo, ndichosadwabwitsanso kuti mamembala a kuchipani anamukhulupila kumusakhanso pa udindo.

A Chakwera ati iwo ndi boma lawo akwanitsa kukweza ndalama yachitukuko kumadela, kubweletsa zipangizo zontchipa za ulimi, kubwezeletsa-nso chikhulupililo kwa omwe amuthandiza dziko lino komanso kukweza mafumu ndikumanga nyumba za apolisi dziko muno.

President Chakwera

Iye amayakhula izi pa m’sonkhano wa ndale ku Area 24 mu m’zinda wa Lilongwe pomwe mwa zina a Chakwera alandila anthu ena m’chipani cha MCP kuchokela ku zipani zina kuphatikizanso yemwe anali mlembi wakale wa chipani cha DPP a Grezeder Jeffrey.

“A Malawi ondifunila zabwino akuona okha ntchito zanga kuphatikizapo kukweza aphunzitsi ndipo ndikulimbikitsa inu nonse ku chipani chathu kuti tigwile ntchito yomema anthu kuti akalembetse kuti adzathe kuvota,” A Chakwera anatelo.

Ndipo iwo adzudzula m’chitidwe omanena za imfa ya yemwe anali wachiwiri wawo a Saulos Chilima pa zifukwa zandale ndipo ati izi ndikupanda umunthu.

“Ine ndikukhulupilira achinyamata komanso amai kuwaika m’maudindo akuluakulu poganizila za tsogolo la dziko lino ndipo ndikutsimikizileni kuti ife ndi mpaka 2030 tilamulilabe,” A Chakwera anatelo.