Thursday, January 16, 2025
No menu items!
spot_img
HomePoliticsChimwendo adzudzula Chipani Cha DPP polankhula Mawu odzetsa mantha pakati pa anthu

Chimwendo adzudzula Chipani Cha DPP polankhula Mawu odzetsa mantha pakati pa anthu

Mlembi wamkulu wachipani cha Malawi Congress (MCP), a Richard Chimwendo Banda, wadzuduzula zimene akuchita atsogoleri ena achipani cha Democratic Progressive (DPP) pomalankhula mawu odzetsa mpungwepungwe komanso mantha pakati pa anthu m’dziko muno.

A Chimwendo Banda ayankhula izi
pa msonkhano wa atolankhani omwe akuchititsa ku Lilongwe.  

Iwo ati mwachitsanzo posachedwapa, a Victor Musowa, omwenso ndi phungu wa Nyumba ya Malamulo waku Mulanje, anauza anthu aku Ndirande mumzinda wa Blantyre kuti asalore aliyense wa MCP kuchititsa msonkhano m’deralo.



Iwo ati a Musowa anena zimenezi patangopita miyezi yochepa mkulu wina wa DPP, a Daudi Chikwanje, atanenanso kuti aliyense wa MCP azitenthedwa.

A Chimwendo ati zimenezi zikuonetseratu kuti DPP ikufuna itabweleranso m’boma pogwiritsa ntchito zipolowe.

A Chimwendo Banda anenetsa kuti chipani chawo sichiopsyezedwa ndi zimene zikuchitikazi, ndipo chiteteza onse otsatira chipani chawo.

Iwo ati chipani cha MCP chipitilira kuchititsa misonkhano pena pali ponse m’dziko muno popanda kuopa chili chonse.

Pa nkhani ya wachinyamata wa chipani cha MCP yemwe anaphedwa ku Ndirande, a Chimwendo Banda apempha apolisi kuti afufuze nkhaniyi kuti amene anachita chiwembuchi  adziwike. 

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments