Chisembwere chakula pakati pa asodzi ndi azimayi ogula nsomba ku Nsanje

By Chisomo Phiri

Mchitidwe wa chisembwere pakati pa asodzi ndi azimayi ogula msomba m’boma la Nsanje akuti wakula kwambiri ndipo ukukolezera kufala kwa kachirombo ka HIV.

Mkulu oona za kulimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito makondomu pogonana m’bomali John Maganizo wanena izi lolemba kwa Sorgin pamwambo okumbukira kugwiritsa ntchito makondomu.

Malingana ndi Maganizo, amayi ambiri ogula msomba amakhudzidwa ndi mchitidwe ogonana ndi asodzi pofuna kupeza msomba mwaulere kwa asodziwa.



Iye wati mchitidwewu wamanga nthenje kumadera komwe kuli madoko ophera msomba monga Magamba ndi Chisamba m’bomali.

Ngati njira imodzi yochepesa kufala kwa kachirombo ka HIV, mimba zosakomzekera komaso matenda opatsirana pogonana, nthambi yazaumoyo m’bomali chaka chatha idagawa makondomu 500,000 m’dera la Sorgin lomwe ndilimodzi mwa madera komwe kuli anthu ochuluka atsopano omwe ali ndi kachirombo ka HIV m’boma la Nsanje.

Poyankhukapo pa nkhaniyi,katswiri wa nkhani zaumoyo pa sukulu ya ukachenjede ya Malawi University of Business and Applied Sciences a Paul Kingstone Mphepo akuti izi zikuchitika chifukwa mabungwe a zaumoyo anatangwanika ndi matenda a Covid-19 komanso kolera.

“Chofunika apa ndi kupereka mwakathithi mauthenga wothandiza anthu kudziteteza ku HIV,” iwo atero.

Nsanje ili ndi anthu 26 000 omwe akulandira mankhwala wotalikitsa moyo a ma ARVs.

Tsiku lokumbukira kufunika kwa makondomu pa dziko lonse limakhala pa February 13 chaka chilichonse.