By Chisomo Phiri
Mtsogoleri wachipani cha Liberation for Economic Freedom (LEF) Dr. David Mbewe wati iye akazavoteledwa kukhala mtsogoleri wadziko lino azabweletsa ngongole zopanda chiwongola dzanja makamaka kwa anthu ochita bizinezi zosiyanasiyana mdziko muno.
Mbewe amayankhula izi dzulo ku Ntaja m’boma la Machinga komwe amakhazikitsa ntchito yake yomanga mlatho wa ndalama zokwana 130 million pa mtsinje wa Mbenjere m’bomali.
Iye anati chiwongola dzanja chomwe anthu ochita bizinezi amapatsidwa akabweleka ndalama kuma banki kapena kuboma chimakhala chochuluka kotelo palibe phindu lomwe iwo amapezamo ndipo kuti izi zikupangitsa ma bizinezi ambiri kulowa pansi.
“Mwachidule chiwongola dzanja ndikubelana. Tangoganizani mupita ku banki kukabweleka K1, 000,000 kuti mutukule bizinezi yanu koma pamwamba pake akukuuzani kuti muonjezerepo K800, 000 ngati chiwongola dzanja. Kumeneku ndikuba.
“Ndikulonjezeni a Malawi anzanga kuti ine kungokhala mtsogoleri wadziko lino, ndili okonzeka kubweretsa ngongole zopanda chiwongola dzanja. Ndikhulupilireni ndipo ndizachita izi,” anatero Mbewe.
Iye anatsindikaso kufunika kosalowetsa ndale patchito zomwe zingatukule dziko lino.
“Tiyeni tigwire ntchito zotukula Malawi posayang’ana kuti awa ndi achipani chanji.Titha kusiyana pa zipani zomwe tili koma tonse ndife a Malawi ndipo ili ndidziko lathu lomwe likufunaka litukulidwe,” Mbewe anaonjezera motero.
M’mawu ake, mfumu yaying’ono Nkhuna yomwe inalinawo pa mwambo otsekulira mlathowu inati iyo ndi anthu ake ndi othokoza kwambiri kaamba ka ntchito yotamandika yomwe a Mbewe abweratsa m’mudzi wawo.
“Mtsinje wa Mbenjere wapha anthu ambiri ndipo ana ambiri alephera maphunziro awo kaamba kamtsinje umenewu. Choncho tikuthokoza a Mbewe potibweretsera mlatho umenewu. Uwu ndi mdalitso waukulu kwa ife ndipo tikupempha a Mbuye Namalenga aziwapatsa moyo wautali a Mbewe,” iwo anatero.
Mtsinje wa Mbenjere udachita malire madera amafumu akulu Liwonde komaso Kawinga.