Sunday, January 19, 2025
No menu items!
spot_img
HomeNationalInkosi Gomani yapempha bata pa nthawi ya Maliro a Chilima

Inkosi Gomani yapempha bata pa nthawi ya Maliro a Chilima

By Linda Kwanjana

Inkosi ya Makhosi Gomani apempha bata pamene Malawi apitilira kukhuza imfa ya Malemu Dr Saulos Klaus Chilima

Mfumu yaikulu ya Maseko Ngoni Inkosi ya Makhosi Gomani 5 yapempha bata ndi mtendere mdziko muno pamene dziko la Malawi likupitilira kukhuza imfa ya yemwe adali wachiwiri kwa Mtsogoleri wadziko lino a Dr Saulos klaus Chilima.

Gomani Kuyankhula pa mwambo wa Maliro a Chilima



Pempholi ladza pamene achinyamata wena usiku wathawu akhala akugenda magalimoto osiyana siyana pamene amapita kuperekeza a Chilima.

Mukulankhula kwawo ku Nsipe , Ntcheu pa mwambo operekeza a Chilima, a Gomani adati ndikofunika kwambiri kusunga bata chifukwa malemu Chilima adali munthu okonda mtendere.

Mfumu yaikulu Gomani idati Maseko Ngoni yataya munthu ofunika kwambiri omwe udali mzati waukulu mboma la Ntcheu komanso dziko lonse la Malawi.

Mfumu Gomani adati a Chilima adzawakumbukira ngati munthu munthu oopa Chauta komanso okonda banja lake.

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments