Thursday, January 16, 2025
No menu items!
spot_img
HomeNationalMHEN yalimbikitsa kufunika kogwila ntchito za umoyo ndi anthu amagulu onse

MHEN yalimbikitsa kufunika kogwila ntchito za umoyo ndi anthu amagulu onse

By Wilfred Golden

Bungwe la Malawi Health Equity Network (MHEN) lati kupezeka kwa anthu amagulu osiyanasiyana m’magulu a amayi omwe amagwila ntchito za umoyo mongodzipeleka m’madela (Mother Care Groups), kukulimbikitsa ntchito yawo yofuna kufikila paliponse ndi uthenga wa kufunika kolondoloza katemela kwa ana osapitilila zaka zisanu.

Wayakhula izi ndi m’modzi mwa omwe akuyendetsa ntchitoyi ku MHEN David Samikwa pomwe anakayendela gulu la amayiwa kwa Sathe m’boma la Lilongwe ndipo iye anati chikhazikitsileni maguluwa anthu ambiri afikilidwa ndi uthengawu kaamba koti panali kulumikizana pa magulu onse.



“M’magulu amenewa timalimbikitsa kuti muzikhala anthu abizinezi, amipingo, atsogoleli a m’dela komanso achinyamata mwa ena, ndipo izi zikuthandizila kuti anthuwa adzitha kufikilana ndikumalimbikitsana mosavuta potengela kuti amadziwa momwe angathe kufikilana molingana ndi mbali yawo,” Samikwa anatelo.

Cholinga cha magulu amenewa komanso mikumanoyi ndichofuna kupititsa patsogolo ntchito yozindikilitsa amayi kufunika kolondoloza akatemela onse kwa ana.

MHEN ikuchita mikumano ndi magulu a amayiwa ku Lilongwe kwa sabata ziwiri pofuna kuchita kalondolondo pa momwe ntchitozi zikuyendela kuyambila nthawi yomwe maguluwa anakhazikitsidwa m’chaka cha 2018.

Mwa makomiti ena omwe akugwila nawo ntchitozi m’madela ndi monga Village Development Committes, Parent Teachers Association, Area Development Committees.

Ndondomekoyi ikuchitika pansi pa thandizo lomwe likupelekedwa ndi bungwe la Global Alliance Vaccine Immunization (GAVI) ndi ukadaulo kuchokela ku unduna wa za umoyo.

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments