Monday, January 20, 2025
No menu items!
spot_img
HomeNationalMphatso Kaonga Akhululukidwa pamulandu opha mwana wake mwangozi

Mphatso Kaonga Akhululukidwa pamulandu opha mwana wake mwangozi

By Chisomo Phiri

Bwalo la milandu ku Nthalire m’boma la Chitipa lamasula Mphatso Kaonga wa zaka 20 pa mulandu opha mwana wake miyezi 21 mwangozi.

Mphatso, msungwana yemwe anamangidwa ali ndi zaka 18 ndipo ataonekera ku bwalo la milandu adavomera mlanduwu ndipo amasungidwa pa ndende ya Chitipa kudikira chigamulo.

Iye amaimilidwa ndi maloya aku Legal Aid Bureau pa mlanduwu ndipo mkufotokoza kwake iye adauza omuyimilirawa kuti adadwalapo malungo othamangira ku bongo zomwe zidachititsa kuti asiye sukulu kaamba kosokonekera m’maganizo.

Mphatso Kaonga



Iye adatenga pakati ali ndi zaka 17 koma sadadziwe yemwe adamupatsa pakatipo. Mwana atabadwa amakhala ndi agogo ake ku Nthalire.

Tsiku lina vuto kakusokonekera mmutu linayambiraso ndipo adatenga mwana wakeyu mkumupha mwangozi.

Ndipo amuyimilira mlanduwu adapereka mbali yawo ya nkhani ku bwaloli, kuti aka nkoyamba kuti Mphatso apalamule mlandu, komanso kuti adali wa chichepere pomwe ankapalamula mlanduwu komanso kuti kuvomera kwake kudaonetsa kukhudzika komanso kuti sanachite mavuvu pa nthawi yonse yomwe wakhala akuzengedwa mlanduwu.

Ndipo oweruza milandu Justice Justuce Kishindo adagwirizana ndi a Legal Aid Bureau pa mfundo zawo ndipo analamula kuti Mphatso amasulidwe koma asakapalamuleso mlandu uliwonse kwa chaka.

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments