Nduna ya Zachuma a Simplex Chithyola apempha amalawu kuti atenge nawo gawp pokonzanso Chuma Chadziko lino

By Simplex Chithyola

Nduna yoona nkhani za Chuma mdziko muno a Simplex Chithyola Banda yayamba ntchito yokambirana ndi anthu amagulu osiyana siyana ndi cholinga chofuna kunva maganizo awo ammene chuma chadziko lino chingapitile patsogolo.

Iwo akumana kale ndi aphungu osiyana siyana, atsogoleri amipingo, mafumu ndinso mabungwe omwe si aboma ku Salima.

Chithyola



Mukulankhula kwawo, a Chithyola ati ndi odandaula kuti boma lapita lija lidatenga ngongole zankhani nkhani zovuta kwambiri kubweza kwake.

Iwo ati nchifukwa chake unduna wawo unaganiza zokonza mkumano kuti ufotokozere anthu okhudzidwa ndimmene nkhani ya zachuma ikuyendela mmdziko muno.

Ena mwa atsogoleri a mabungwe omwe anali nawo ku mkumanowu ndi monga a Silvester Namiwa a CDED, Bon Kalindo, Robert Mkwezalamba, a Lucky Mbewe ndi ena ambiri.

Komanso nduna zaboma a Sam Kawale , Richard Chimwendo Banda, ndi a Jacob Hara anali nawonso kumkumanowu.