Nyamazikuzikulu Ken Zikhale Ng’oma Zilibe Manjenje

Wolemba: Leonard Kavwenje


Mmodzi mwa mamembala a komiti yaikulu ya chipani cholamula boma cha Malawi Congress (MCP) yemwenso ndi Phungu wa Nyumba ya Malamulo Kummwera kwa Nkhata Bay yemwenso ndi nduna ya zachitetezo cha mdziko Dr. Ken Zikhale Reeves Ng’oma apempha Amalawi onse kugwira ntchito ndi boma popititsa patsogolo chitukuko cha dziko lino.

Poyankha lamya yawo ya mmanja kuchokera pa mchombo pa fuko la Malawi a Ng’oma ati, “Chilungamo ndi chakuti Malawi sangachoke mu umphawi ndi njala ngati nzika zikusemphana pa masomphenya. Ndikupempha Amalawi tonse tigwire ntchito limodzi ndi mtsogoleri Dr. Lazarus McCarthy Chakwera komanso chipani chachikulu cha MCP. Tikuyenera kuchirimika pa ntchito za ulimi, zokopa alendo komanso migodi kuti tonse pamodzi tisimbe lokoma. Ndale zamakedzana zokokanakokana sizititengera kulikonse.”

Wolemekezeka a Zikhale kuyankhula pa Msonkhano



Atafunsidwa pa za chisankho cha chaka cha mawa a Ng’oma ati, “Achimwene MCP siyikuopa aliyense. Ulendowu ndi wakutsogolo. Ngati inu mukupanga za otsutsa boma cheke cheke thwa muchedwa nazo. Ndikuuzeni chilungamo MCP ikutenganso boma chaka cha mawa. Amalawi adazindikira pano. Sakusintha chipani cholamula boma. Sakusintha zipani zotsutsa. Ngati muli ndi foni yaikulu tengani sikirinishoti. MCP idzasesa mavoti 70 pa 100 alionse. Amalawi sakufuna phokoso koma ntchito zokoma za Dr. Lazarus McCarthy Chakwera kuti zipitirire.”

Wayabwa kuposa chitedze Zikhale Ng’oma!