PSI isumilidwa pochita mdulidwe kwa ana 312 popanda chilolezo chamakolo

By Sylvester Chibwana

Ana 312 a m’boma la Phalombe asumira bungwe la Population Services International (PSI) lomwe tsopano likudziwika kuti Family Health Services (FHS) kaamba kowachita mdulidwe popanda chilolezo cha makolo awo.

Woyamba amene akamang’ala kubwalo la Midima ku Limbe mumzinda wa Blantyre ndi a Damson Esimey, omwe amayang’anira mnyamata wina, Enock Kachala.

Iwo adandaula kuti bungwelo lidapititsa ku mpeni mwanayo ndi anzake ena 311 kwa T/A Mkando m’boma la Phalombe asanawapatse uthenga ndi uphungu wokwanira.



A Dalitso Chimbe ndiwo akuimira anawo omwe akufuna chipepeso kaamba kovulazidwa, kuikidwa mu ululu ndi kupatsidwa chilema mosemphana ndi gawo 30 la malamulo oteteza ana.

Pambali pa chipepeso, anawo akufunanso kuti PSI ilipire ndalama zimene agwiritse ntchito nthawi yomwe mlanduwo ukhale ukumvedwa kubwalolo.

Iwo akutinso mwa zina, cholinga cha mdulidwewo sichidali kuchiza anawo kapena kutsatira miyambo ya makolo ngakhalenso chipembedzo.

M’zikalata zosumazo, anawo akuti izi zidachitika pakati pa chaka cha 2021 ndi 2022 pomwe adadulidwa popanda chilolezo cha makolo pomwe adangokopeka ndi nyimbo zoseweredwa pa chimkuzamawu cha galimoto ya PSI imene inkazungulira m’bomalo kuwamema kuti akalandire mdulidwe pa chipatala chaching’ono cha Migowi.

Koma woimira PSI a Francis Kaduya ati apempha bwalolo kuti lisamvere izi chifukwa ena amene akufuna chipepeso akutero kaamba ka ukathyali wongofuna kupeza chipepeso posayenera.