Sunday, January 19, 2025
No menu items!
spot_img
HomeNewsRas Chikomeni Chirwa akugulitsa chamba kuti apeze ndalama zoyimila upulezidenti 2025

Ras Chikomeni Chirwa akugulitsa chamba kuti apeze ndalama zoyimila upulezidenti 2025

By Chisomo Phiri

Yemwe akufuna kudzayimira nawo pampando wa pulezidenti pa chisankho cha 2025 a Ras Chikomeni Chirwa wati wayamba kugulitsa chamba kuti apeze ndalama zomwe zimafunikira kupereka ku bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) kuti munthu ayimire nawo pa chisankho .

A Chirwa atsimikiza izi kuyilesi ya Zodiak ponena kuti mpingo wawo wama Ras unalandira chiphaso  chowavomereza kugulitsa chamba kwa chaka chimodzi kuchokera kubungwe lowona za ulimiwu la Cannabis Regulatory Authority (CRA) ndipo ayamba kugulitsa chambachi kuti apeze ndalama zokwanira.

Presidential candidate Ras Chikomeni Chirwa



Iwo ati,akugulitsanso ma T-shirt kuti apeze ndalama zokwanira zogwiritsa ntchito kukonzekera chisankho cha 2025 ndipo wapemphanso aMalawi kuti amuthandize.

“Ndizoona ndipo khumbo lathu ndikupeza ndalama zoti zitithandize pa zisankho za chaka chamawa,” atero a Chirwa.

Katswiri pa nkhani za ndale a  Chimwemwe Tsitsi wayamikira a Ras Chikomeni kaamba koyamba pawokha kusaka ndalama ndipo awalangizanso kuti afikira anthu omwe ali ndikuthekera kowathandiza.

Muzisankho za 2019, a Chirwa adalephera kupikisanawo pa mpando waupulesidenti atalephera kupeleka ndalama yomwe a MEC amafuna kuti aliyese opikisananawo pa mpandowu apeleke.

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments