Rev Kamuyambeni ndi A Samson Mithenga akana malipoti oti alowa UTM

Wolemba Mtolankhani Wathu

Mamembala a chipani cha Malawi Congress (MCP) m’busa Mwai Kamuyambeni komanso a Samson Nthenga atsutsa malipoti oti alowa chipani cha UTM.

Izi zikutsatira chithunzi chomwe awiriwa anajambulitsa ndi mtsogoleri wachipani cha UTM, a Dalitso Kabambe kunyumba kwao Lachiwiri sabata ino.

Awiriwa avomera kuti anajambulitsa chithunzicho pomwe anawaitana monga munthu ndi mzache poti anayamba kucheza kalekale.

Iwo ati anali odabwa kuti pomalizira kwakucheza kwao a Kabambe anawapempha kuti agwire nao ntchito ndipo m’busa Kamuyambeni ndi a Nthenga ati anangoti awayankhabe.

Rev Kamuyambeni ndi a Samson Mithenga



Titawafunsa ati mauwa anali kukana ndithu kulowa chipani cha UTM ndipo iwo ali pambuyo pachipani cha MCP.

A Kamuyambeni ati iwo adzaimira ngati phungu wa MCP dera lina m’boma la Ntcheu.

O