Saturday, January 25, 2025
No menu items!
spot_img
HomeNationalSitidawachotse ndife a Mutharika muchisankho cha 2020-HRDC yatsutsa kwa mtuwagalu

Sitidawachotse ndife a Mutharika muchisankho cha 2020-HRDC yatsutsa kwa mtuwagalu

By Chisomo Phiri

Limodzi mwa mabungwe akuluakulu omenyera maufulu awanthu mdziko muno la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) latsutsa kwa mtuwagalu zomwe wanena mtsogoleri wa chipani chakale cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP) a Peter Mutharika kuti kuti chipani chomwe chikulamula panopa cha Malawi Congress Party (MCP) chidagwiritsa ntchito bungweli powachotsa m’boma muchisankho cha mu 2020.

Dzulo, a Mutharika anabwerezanso izi pa msonkhano wa atolankhani omwe anachititsa ku nyumba yawo m’boma la Mangochi.

Madalitso Banda



Koma mkulu wa HRDC kum’mawa kwa dziko lino a Madalitso Banda auza a Mutharika kuti apange zokonza chipani chawo m’malo momalimbana ndi bungweli.

A Banda anenetsa kuti zomwe analankhula a Mutharika nzabodza popeza HRDC siyipanga nawo za ndale.

“Mzovetsa chisoni kuti mtsogoleri wakaleyu akusungira mangawa bungwe la HRDC zomwe Amalawi sangakonde kuti adzakhale ndi mtsogoleri osadziwa kuyanjanitsa anthu  ngati a Mutharika,” awonjezera choncho a Banda.

HRDC linali limodzi mwa mabungwe omwe adatsogolera zionetsero za kathithi zotsutsana ndi zotsatira za chisankho cha mu 2019 ponena kuti sichinayende bwino.

Panthawiyo, bungwe loyendetsa chisankho la MEC, motsogozedwa ndi wapampando wake wakale Dr. Jane Ansah lidalengeza kuti a Mutharika ndi omwe adapambana.

Koma bwalo la milandu lidagamula kuti panali zotsamwitsa zina ndipo a Malawi adaponyanso voti komwe adasankha a Lazarus Chakwera a MCP ngati mtsogoleri wa dziko.

A Mutharika panopa awonetsa chidwi chawo chozapikisananawo pa mpando wa mtsogoleri wadziko lino mchisankho cha 2025.

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments