By Chisomo Phiri
Yemwe akuzapikisananawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko lino muzisankho za chaka chamawa Eddie Dada Gaddafi General Longwe wati ndi okhudzidwa ndi momwe ndale mdziko muno zikuyendera ponena kuti sizikuphula mu umphawi wa dzaoneni omwe a Malawi akukumananawo.
Longwe yemwe akuzayima payekha muzisankho zikudzazi wati a Malawi anamizidwa kokwana ndipo kuti nthawi tsopano yakwana yoti amasulidwe.
Iye wati alibe chikhupiliro choti zinthu zingadzayende bwino mdziko muno ngati sipakhala kusintha kosankha atsogoleri moyang’ana mitundu komaso zipani.
Longwe wati mzodandaulitsa kuti m’malo muyika chidwi pa zinthu zomwe zingatukule dziko lino, atsogoleri akuchedwa ndi kupanga zipani za ndale.
“Pali chiopsyezo chachikulu m’dziko muno ndipo ngati sitichitapo kanthu a Malawi ambiri apitilira kukhala pa umphawi wadzaoneni.
“Tangoganizani,a Malawi akusowa zinthu zofunikila pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku ndipo ena akufa mzipatala kaamba kosowa mankhwala.Izitu mzovetsa chisoni kwambiri,” watero Longwe.
Iye wati pali ndondomeko zingapo zomwe akuona kuti akazawina chaka chamawa zizamuthandiza kubwezeletsa chuma cha dziko lino mchimake monga kuonetsetsa kuti nkhani za ulimi zikuyenda mwa makono ndicholinga choti alimi azizapeza zokolola zochuluka, kusiya kubwereka ndalama zakunja,kuchepetsa kuononga ndalama zadziko pazinthu zosapindulira a Malawi komanso kuthetsa katangare posatengera kudziwana kapena mitundu.